Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 10:2 - Buku Lopatulika

2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu oipa amazunza anthu osauka modzikuza. Akodwe m'misampha yotcha iwo omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka, amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 10:2
18 Mawu Ofanana  

Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.


Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse.


Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zanga kuti ndisamalire malemba anu.


Odzikuza anandipangira bodza: Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.


Odzikuza anandikumbira mbuna, ndiwo osasamalira chilamulo chanu.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.


Phazi la akudzikuza lisandifikire ine, ndi dzanja la oipa lisandichotse.


Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.


Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.


Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.


Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?


Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.


Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;


Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;


pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe mu Ejipito kukhala m'menemo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa