Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 9:20 - Buku Lopatulika

20 Muwachititse mantha, Yehova; adziwe amitundu kuti ali anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Muwachititse mantha, Yehova; adziwe amitundu kuti ali anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Inu Chauta, aopseni anthuwo. Akunjawo adziŵe kuti iwo ndi anthu chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova; mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 9:20
14 Mawu Ofanana  

Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m'chigwa cha Zefati ku Maresa.


Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu.


Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Iye adzadula mzimu wa akulu; akhala woopsa kwa mafumu a padziko lapansi.


Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.


Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.


Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,


Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.


Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa