M’mawu a Mulungu, amanena kuti chigololo chimachitika munthu wokwatira kapena wokwatiwa akagonana ndi munthu wosakhala mkazi kapena mwamuna wake. Ichi ndi tchimo chomwe chimatsutsana ndi kuyera kwa ukwati ndi thupi lathu, ndipo Mulungu adzachiweruza.
Masiku ano, kusakhulupirika m’banja kwafala kwambiri, ngakhale pakati pa Akhristu, ndipo izi zikuwononga mabanja ambiri. Ndikofunika kuti tonse, tisunge mitima yathu yoyera ndikukhala maso kuti tisagwere m’misampha ya dziko lapansi, lomwe limayesa kutipangitsa kuona ngati zinthu izi ndi zachibadwa.
Ndikofunikanso kuti tisalole achinyamata athu kuonera kapena kumva uthenga wokhudza kusakhulupirika, chinyengo, uhule, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndi zinthu zina zonyansa, chifukwa zinthu zimenezi zingawabweretsere mavuto aakulu m’miyoyo yawo ndikuwasokoneza pa cholinga cha Mulungu pa miyoyo yawo. M’malo mwake, tiwalimbikitse kuti azikonda ndi kusamalira mabanja awo amene Mulungu wawapatsa, ndipo akamayesedwa, azithamangira kwa Khristu kuti akapemphe thandizo.
Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.
Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.
Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.
Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.
Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.
Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;
Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.
Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo;
Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo. Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, ndi kumtulutsa m'nyumba mwake.
Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;
Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,
Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana. kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Chifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamzinda kukamenyana nao? Simunadziwe kodi kuti apalingawo adzaponya? Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa. Chomwecho mthengawo unamuka, nufika, nudziwitsa Davide zonse Yowabu anamtumiza. Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatipambana natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata. Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa. Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere. Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake. Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita. Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti? Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.
Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa. Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake; wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake.
Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta. Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse. Mayendedwe ake atsikira kuimfa; mapazi ake aumirira kumanda;
Imwa madzi a m'chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja, ndi mitsinje ya madzi m'makwalala? Ikhale ya iwe wekha, si ya alendo okhala nawe ai. Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka. ukasunge zolingalira, milomo yako ilabadire zomwe udziwa. Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere, ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?
Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere. Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali. Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake? Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.
Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.
Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake. Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru; mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.
madzi akuba atsekemera, ndi chakudya chobisika chikoma. Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko; omwe achezetsa utsiru ali m'manda akuya.
Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza. Pakuti abisalira ngati wachifwamba, nachulukitsa anthu a chiwembu.
Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.
ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.
Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.
Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.
Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama. Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.
Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m'nyumba za adama. Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wake.
Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu ina imene simunaidziwa,
Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.
chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.
Pakuti anachita chigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao aamuna amene anandibalira, kuti athedwe.
Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake;
Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu aakazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo. Sindidzalanga ana anu aakazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.
Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.
Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.
Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako. Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,
Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m'kati, nkudetsa munthu.
Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.
Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m'chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati, Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye. Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani. Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhale akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu? Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse. Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu. Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu. Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu. Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu. ananena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkuchita chigololo. Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite. Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwe ife m'chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu. Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadze kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine. Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga. Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza. Koma Ine, chifukwa ndinena choonadi, simukhulupirira Ine. Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji? Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu. Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda? Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa. Koma m'chilamulo Mose anatilamula, tiwaponye miyala otere. Chifukwa chake Inu munena chiyani za iye?
Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi? Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.
anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.
Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna, komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.
kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;
Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira; pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.
Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro, mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa. Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo. Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa. Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.
Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.
Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano. Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake. Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m'chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake.
ndipo sanalape mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.
Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.
Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru;
Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?
Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama. Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama? Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?
Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzachita zigololo naye, ndi iyenso nao. Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wachigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.
Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere.
Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala mu Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.
Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira, ndi kuti, Palibe diso lidzandiona; navala chophimba pankhope pake.
Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Tiro, ndipo iye adzabwerera kumphotho yake, nadzachita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.
Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri;
Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;
Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma.
Ha? Mtima wako ngwofooka, ati Ambuye Yehova, pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi wachigololo wouma m'maso.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.