Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 3:1 - Buku Lopatulika

1 Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta akuti, “Munthu akasudzula mkazi wake, mkaziyo nkuchoka, nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumtenganso mkaziyo? Kodi atachita zotero, sindiye kuti dzikolo laipitsidwa kwambiri? Tsono iwe Israele, wachita zadama ndi abwenzi ambiri. Kodi ungabwererenso kwa Ine?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Ngati munthu asudzula mkazi wake ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo? Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri? Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri. Komabe bwerera kwa ine,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:1
34 Mawu Ofanana  

nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.


Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthawi zonse.


Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.


Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;


Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.


Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako mu Basani; nufuule mu Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha.


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.


Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.


Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa.


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, aakulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.


Ha? Mtima wako ngwofooka, ati Ambuye Yehova, pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi wachigololo wouma m'maso.


Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova:


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.


Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake;


Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.


Chifukwa chake uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu.


Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye kalata yachilekaniro:


pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.


Koma mkazi wake wamng'ono anachita chigololo akali naye, namchokera kunka kunyumba ya atate wake ku Betelehemu ku Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa