Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 2:37 - Buku Lopatulika

37 Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Mudzatuluka kumeneko aliyense atagwirira manja ku mutu. Ine Chauta ndidaŵakana amene inu mumagonerapo, ndipo anthuwo sadzakuthandizani mpang'ono pomwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Mudzachokanso kumeneko manja ali kunkhongo. Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira, choncho sadzakuthandizani konse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:37
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake.


Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.


Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ake, ndi malipenga oliza nao chokweza, kukulizirani inu chokweza. Ana a Israele inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.


Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri woopsa udzakuponderezani pansi.


Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao.


Chifukwa cha nthaka yochita ming'alu, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, afunda mitu yao.


Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake.


Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.


Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako mu Basani; nufuule mu Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha.


Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso mu Yuda.


ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?


Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo chabe; kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.


Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa