Hoseya 3:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Pitanso, ukakonde mkazi wachigololo amene ali ndi chibwenzi chake. Umkonde monga momwe Ine Chauta ndimakondera Israele, ngakhale iyeyo amapembedza milungu ina, ndipo amakonda kuitsirira nsembe za mphesa zabwino zoumika.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.” Onani mutuwo |