Hoseya 3 - Buku LopatulikaAkwatiranso mkazi woipa, kufaniziranso zochita ana a Israele 1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma. 2 M'mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu a siliva, ndi homeri ndi leteki wa barele; 3 ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe. 4 Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi; 5 atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi