Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 2:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Israele ndidzamubzala m'dziko kuti akhale wanga. Ndidzaonetsa chikondi kwa ‘Sakondedwa’ uja. Anthu amene ndinkaŵatchula ‘Si-anthu-anga,’ ndidzaŵauza kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Ndinu Mulungu wathu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 2:23
33 Mawu Ofanana  

Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Akulu adzafumira ku Ejipito; Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.


M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.


Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake: aweta zake pakati akakombo.


Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Ndipo inu mudzakhala anthu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.


ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;


pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.


Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.


Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse.


Adzafuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisraele tikudziwani.


Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukira m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga chikondwerero cha Misasa.


Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso:


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa