Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 7:26 - Buku Lopatulika

26 ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa, mkazi amene ali ngati khoka, amene mtima wake uli ngati khwekhwe, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo, koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 7:26
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.


mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?


Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?


Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;


M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.


Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.


Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.


Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko; omwe achezetsa utsiru ali m'manda akuya.


Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa