Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 7:4 - Buku Lopatulika

4 Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa woocha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Onsewo ndi osakhulupirika, udani wao ndi wonyeka ngati moto wamuuvuni, umene mphikabuledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanyanga mtanda wa buledi mpaka utafufuma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Onsewa ndi anthu azigololo, otentha ngati moto wa mu uvuni, umene wophika buledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 7:4
10 Mawu Ofanana  

Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu.


Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.


Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa