Yeremiya 23:10 - Buku Lopatulika10 Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo. Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko mwagwa chilala, mabusa akuchipululu auma. Amene amangothamangira zoipa, amalimbikira kuchita zosalungama. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Dziko ladzaza ndi anthu achigololo; lili pansi pa matemberero. Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma. Aneneri akuchita zoyipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. Onani mutuwo |