Ndikukuuzani inu, palibe chofanana ndi kudzionera wekha. Mukakhala ndi Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku, mumapeza njira yabwino yolankhulira uthenu kwa ena. Uthenu umenewu ukhoza kusintha miyoyo ya anthu ambiri.
Palibe chomwe chimakhudza mtima wa munthu kuposa uthenu womwe wabwera chifukwa choona zinthu ndi maso ako. Komabe, Mzimu Woyera ndiye chinsinsi chachikulu. Iye ndiye amadziwa zonse ndipo amatipatsa nzeru zomwe timafunikira kuti timvetse bwino Mawu a Mulungu.
Tisamadalire kwambiri maganizo athu okha kapena nkhani za anthu ena. Zinthu zimenezi sizingatithandize kulankhula bwino uthenu ngati sitinazione tokha. Tikamadalira maganizo athu okha, nthawi zina tingasowe choti tinene.
Mzimu Woyera akufunitsitsa kutiphunzitsa lero. Mulole kuti akuthandizeni kumvetsa ndi kufotokoza uthenu wanu m'njira yoti ena amvetse.
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu; m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende,
Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.
Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chilombocho; pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.
Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo, Ndipo Nowa anabala ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi. Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi. Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m'chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja. Kupanga kwake ndi kotere: m'litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwake mikono makumi asanu, m'msinkhu mwake mikono makumi atatu. Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu. Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa. Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi. kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo. Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo. Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita. Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri. Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.
Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.
Koma za mizinda ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma; koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;
Ndipo Yefita anawindira Yehova chowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa, ndipo kudzali kuti chilichonse chakutuluka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kuchokera kwa ana a Amoni, chidzakhala cha Yehova, ndipo ndidzachipereka nsembe yopsereza.
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.
Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kamvulumvulu, nati, ndi kuilembera malire anga, ndi kuika mipikizo ndi zitseko, ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza? Kodi walamulira m'mawa chiyambire masiku ako, ndi kudziwitsa mbandakucha malo ake; kuti agwire malekezero a dziko lapansi, nakutumule oipa achokeko? Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa chosindikiza, ndi zonse zibuka ngati chovala; ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone, ndi dzanja losamulidwa lithyoledwa. Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni? Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe? Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa? Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziwa chonse. Ili kuti njira yomukira pokhala kuunika? Ndi mdima, pokhala pake pali kuti, Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mau opanda nzeru? kuti upite nao kumalire ake, kuti uzindikire miseu ya kunyumba yake? Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo, ndi masiku ako achuluka kuwerenga kwao. Kodi unalowa m'zosungiramo chipale chofewa? Kapena unapenya zosungiramo matalala, amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo? Njira ili kuti yomukira pogawikana kuunika, kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa padziko lapansi? Ndani anachikumbira mchera chimvula, kapena njira ya bingu la mphezi, kuvumbitsa mvula padziko lopanda anthu, kuchipululu kosakhala munthu, kukhutitsa thengo la kunkhwangwala, ndi kuphukitsa msipu? Kodi mvula ili naye atate? Kapena wabala ndani madontho a mame? Chipale chinatuluka m'mimba ya yani? Ndi chisanu chochokera m'mwamba anachibala ndani? Udzimangire m'chuuno tsono ngati mwamuna; ndikufunsa, undidziwitse. Madzi aundana ngati mwala, ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi. Kodi ungamange gulu la Nsangwe? Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana? Ungatulutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao? Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ake? Kodi udziwa malemba a kuthambo? Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao padziko lapansi? Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo, kuti madzi ochuluka akukute? Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke, ndi kunena nawe, Tili pano? Ndani analonga nzeru m'mitambomo? Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha? Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani, pokandika fumbi, ndi kuundana zibuma pamodzi? Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama? Ndi kukwaniritsa chakudya cha misona, Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.
kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;
Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.
Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti ungafanane nacho iwe wekha. Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti asadziyese wanzeru.
Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo; Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi. Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.
Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo; ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.
Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri. Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto. Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu. Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.
Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena. Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.
Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere padziko lapansi; sindinadzere kuponya mtendere, koma lupanga.
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.
Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.
Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.
Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeze; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima; monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.
Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye. Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho. Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo. Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu. Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.
Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?
Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa. Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine. Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.
kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye,
pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera, nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza, koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.
Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.
Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.
Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.
Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao. Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.
diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo.
Akalimbana wina ndi mnzake, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wake m'dzanja la wompandayo, nakatulutsa dzanja lake, ndi kumgwira kudzivalo; pamenepo muzidula dzanja lake; diso lanu lisamchitire chifundo.
Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.
Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.
Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu. Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.
nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.
Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa. Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anatuluka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa chigwa, ndicho chodzala ndi mafupa; M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chilili, gulu la nkhondo lalikulukulu ndithu. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa. Chifukwa chake, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu mutuluke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israele. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova potsegula Ine kumanda kwanu, ndi kukweza inu kukutulutsani m'manda mwanu, anthu anga inu. Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kuchichita, ati Yehova.
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu? koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine. Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake: pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatse Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetse Ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandire Ine; wamaliseche ndipo simunandiveke Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadze kundiona Ine. Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu? Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine. Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.
Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye. Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine. Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu. Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha. Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine. Ndipo tsopano ndakuuzani chisanachitike, kuti pamene chitachitika mukakhulupirire. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi. mu Frijiya, ndiponso mu Pamfiliya, mu Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu. Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani? Koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero. Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu mu Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga. Pakuti awa sanaledzere monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku; komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yowele, Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera. Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi; Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera. Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa. Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha; ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika; yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo. Pakuti Davide anena za Iye, Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse; chifukwa ali padzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike; mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo. Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde, munandidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu. Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake; iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwe m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde. Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva. Pakuti Davide sanakwere Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako. Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika. Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale? Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.
Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.
Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu; chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.
koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.
Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.
Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.
pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.
Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene. Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde. Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa. Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Pakuti m'nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa.
Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.
Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.
koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu.
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake; koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi? Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu. Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.
Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.
Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.
Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.
Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.