Chivumbulutso 3:5 - Buku Lopatulika5 Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Iye amene alakika adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake. Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.