Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 2:1 - Buku Lopatulika

1 Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsiku linanso pamene ana a Mulungu anabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anabwera nawo limodzi kudzadzionetsa pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 2:1
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.


Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pao.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo.


muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.


Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa