Yeremiya 7:18 - Buku Lopatulika18 Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Ana akutolera nkhuni, atate akusonkha moto, akazi akukanda ufa kuti aphike makeke, kuchitira ulemu amene amati ndi mfumukazi yakumwamba. Iwowo amathira nsembe yazakumwa kwa milungu ina, kuti andipsetse mtima. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. Onani mutuwo |