Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 7:17 - Buku Lopatulika

17 Kodi suona iwe chimene achichita m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Kodi suona iwe chimene achichita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Kodi sukuwona zimene zikuchitika m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya m'Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:17
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu.


Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.


Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.


Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.


Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.


Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.


Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa