2 Samueli 24:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Nthaŵi ina Chauta adaŵakwiyiranso Aisraele, choncho adautsa mtima wa Davide kuti aŵavutitse. Adamuuza kuti, “Pita ukaŵerenge Aisraele ndi Ayuda.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.” Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.