2 Samueli 24:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.” Onani mutuwoBuku Lopatulika1 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Nthaŵi ina Chauta adaŵakwiyiranso Aisraele, choncho adautsa mtima wa Davide kuti aŵavutitse. Adamuuza kuti, “Pita ukaŵerenge Aisraele ndi Ayuda.” Onani mutuwo |
Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto.