1 Akorinto 15:29 - Buku Lopatulika29 Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Tsono ngati kulibe kuuka kwa akufa, kodi iwo amene akubatizidwa chifukwa cha akufa, adzatani? Ngati akufa saukitsidwa nʼkomwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa mʼmalo mwawo? Onani mutuwo |