Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Tsono adaŵachitira maere anthu aŵiriwo. Maerewo adagwera Matiasi, ndipo iyeyo adawonjezedwa pa gulu lija la atumwi khumi ndi mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:26
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.


Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo;


Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.


Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake; koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.


Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse.


Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazele.


Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.


Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.


Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi.


Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri mu Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;


Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu mu Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga.


Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.


Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.


Ndipo linga la mzinda linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa