Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 27:46 - Buku Lopatulika

46 Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau akulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Ndipo nthawi ili ngati 3 koloko, Yesu analira mofuwula nati, “Eloi, Eloi, lama sabakitani!” Kutanthauza kuti, “Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, mwandisiyiranji Ine?”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:46
9 Mawu Ofanana  

Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?


ndi kuti, Wamsiya Mulungu. Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?


Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya.


Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?


Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau aakulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa