Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 1:3 - Buku Lopatulika

3 koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Komabe ndakonda Yakobe, koma Esau ndadana naye. Dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu, dziko limene ndidampatsa ndalisandutsa la nkhandwe zam'chipululu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 koma ndinamuda Esau, ndipo dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu ndipo cholowa chake ndasiyira ankhandwe a mʼchipululu.”

Onani mutuwo Koperani




Malaki 1:3
26 Mawu Ofanana  

Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.


Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.


Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye.


Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.


Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.


Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?


Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.


Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende; koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzavumbulutsa zochimwa zako.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.


Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa,


Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao.


Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse.


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa