Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 1:4 - Buku Lopatulika

4 Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mwina Aedomu adzanena kuti, “Mulungu adapasula nyumba zathu, komabe ife tidzazimanganso.” Koma Chauta Wamphamvuzonse adzati, “Alekeni amangenso, Ine ndidzazigwetsanso. Anthu adzalitchula dziko loipa, la anthu amene Chauta adaŵatemberera mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mwina Edomu nʼkunena kuti, “Ngakhale taphwanyidwa, tidzamanganso mʼmabwinja.” Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Iwo angathe kumanganso, koma Ine ndidzazigwetsanso. Iwo adzatchedwa dziko loyipa, la anthu amene Yehova wayipidwa nawo mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 1:4
37 Mawu Ofanana  

Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso; amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira.


Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;


Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.


Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.


Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wake udzakwera nthawi zonse; m'mibadwomibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi.


Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.


Ndipo chilipo chiyembekezero cha chitsirizo chako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao.


Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.


Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?


Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.


Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.


Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira?


Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.


Ndipo ndidzalibwezera Edomu chilango mwa dzanja la anthu anga Israele; ndipo adzachita mu Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera chilango kwanga, ati Ambuye Yehova.


Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndachinena, ati Ambuye Yehova.


Ndidzapasula mizinda yako, nudzakhala lachipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m'mizinda mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;


Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.


Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.


Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikulu ichite mpata, ndi nyumba yaing'ono ichite mindala.


Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?


Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.


Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse.


koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu.


Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa