Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 11:7 - Buku Lopatulika

7 Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nkhumba: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale ziboda zake nzogaŵikana ndipo mapazi ake ngogaŵikananso, koma siibzikula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 11:7
11 Mawu Ofanana  

amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;


Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatanetsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi chonyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.


Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika chiboda, mumuyese wodetsedwa.


Nyama yake musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfumu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba.


Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.


ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa