Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 14:26 - Buku Lopatulika

26 Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 “Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga.

Onani mutuwo Koperani




Luka 14:26
18 Mawu Ofanana  

Ndidana nao ndi udani weniweni, ndiwayesa adani.


Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.


Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza.


Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo Iye anapotoloka, nati kwa iwo,


Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.


Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,


Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa