Ndipo Yehova anapatsa Solomoni nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, iwo awiri napangana pamodzi.
Masalimo 127:1 - Buku Lopatulika Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe. |
Ndipo Yehova anapatsa Solomoni nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, iwo awiri napangana pamodzi.
Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite.
Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.
nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.
Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri, monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.
Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.
Alonda akuyendayenda m'mzinda anandipeza: Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
Alonda akuyenda m'mzinda anandipeza, nandikantha, nanditema; osunga makoma nandichotsera chophimba changa.
Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.
Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.
Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,
Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala mu Babiloni.
Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzake, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzake, kukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mzinda wake wagwidwa ponsepo;
ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.
Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.
Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israele, kulizonda dziko.