Mlaliki 9:11 - Buku Lopatulika11 Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Ndidaonanso pansi pano kuti opambana pa kuthamanga si aliŵiro okhaokha, opambana pa nkhondo si amphamvu okhaokha, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru okhaokha. Olemera si odziŵa zambiri okhaokha, ndipo si anthu aluso okhaokha amene anzao amaŵakomera mtima. Onsewo mwai umangoŵagwera pa nthaŵi yake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano: opambana pa kuthamanga si aliwiro, kapena opambana pa nkhondo si amphamvu, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru, kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri, kapena okomeredwa mtima si ophunzira; koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake. Onani mutuwo |