Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:12 - Buku Lopatulika

12 Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala mu Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala m'Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kwezani mbendera yankhondo ndipo muwononge malinga a Babiloni. Mulimbitse oteteza, muike alonda, mukonzekere kulalira. Pakuti Chauta watsimikiza, ndipo adzachitadi zimene adanena za anthu a ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni! Limbitsani oteteza, ikani alonda pa malo awo, konzekerani kulalira. Pakuti Yehova watsimikiza ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:12
18 Mawu Ofanana  

Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.


Kwezani mbendera paphiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akulu.


Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; masiku otsiriza mudzachidziwa bwino.


Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Yehova watsegula pa nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi ntchito m'dziko la Ababiloni.


Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe.


Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo.


Yehova wachita chomwe analingalira; watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale; wagwetsa osachitira chisoni; wakondweretsa adani pa iwe, wakweza nyanga ya amaliwongo ako.


ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.


Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'chuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.


Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m'mzinda kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mzinda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa