Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 127:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 127:1
35 Mawu Ofanana  

Yehova anamupatsa Solomoni nzeru monga momwe analonjezera. Panali ubale wa mtendere pakati pa Solomoni ndi Hiramu, ndipo awiriwa anachita pangano.


Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”


Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha.


Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.”


Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.


Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti?


Ndinakondwera atandiwuza kuti, “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”


Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba.


Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli,


Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.


Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota.


Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo, Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.


Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda, dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.


Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.


Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano: opambana pa kuthamanga si aliwiro, kapena opambana pa nkhondo si amphamvu, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru, kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri, kapena okomeredwa mtima si ophunzira; koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.


Alonda anandipeza pamene ankayendera mzinda. “Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?”


Alonda anandipeza pamene ankayendera mzindawo. Anandimenya ndipo anandipweteka; iwo anandilanda mwinjiro wanga, alonda a pa khoma aja!


Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira; ndimawuthirira nthawi zonse. Ndimawulondera usana ndi usiku kuti wina angawononge.


Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu, onse ndi opanda nzeru; onse ndi agalu opanda mawu, samatha kuwuwa: amagona pansi nʼkumalota amakonda kugona tulo.


Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda; sadzakhala chete usana kapena usiku. Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake musapumule.


Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni! Limbitsani oteteza, ikani alonda pa malo awo, konzekerani kulalira. Pakuti Yehova watsimikiza ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.


Othamanga akungopezanapezana, amithenga akungotsatanatsatana kudzawuza mfumu ya ku Babuloni kuti alande mzinda wake wonse.


Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, ndiye kuti kulalikira kwathu nʼkopanda ntchito, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso ntchito.


Choncho kuphatikiza iye wodzala ndi iye wothirira, onse sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amakulitsa zinthu.


Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe.


Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.


Mfumu ya Yeriko inawuzidwa kuti, “Aisraeli ena afika mu mzinda muno usiku uno kudzazonda dziko.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa