Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


102 Mau a m'Baibulo Okhudza Ngongole

102 Mau a m'Baibulo Okhudza Ngongole

Choyamba, sungani mtima wanu. Muyenera kupewa chilichonse chomwe sichikukulimbikitsani. N'zoona kuti zinthu zonse ndi zovomerezeka kwa inu, koma sikuti zonse zimakukomerani. Choncho, samalani ndi zisankho zanu zonse, pemphani Mulungu nzeru ndipo musalole kuti maganizo anu akulamulireni, chifukwa angakutsogolereni panjira yoipa.

Nthawi zambiri mdani adzakupatsani mayankho omwe nthawi ya mavuto angawoneke ngati oyenera, koma samalani! Mapeto ake nthawi zonse amatsogolera ku imfa. Ngongole si njira yabwino yothetsera mavuto. M'malo mwake, pitani kwa Mulungu ndipo mudzapeza thandizo lanu panthawi yake. Yesu amadziwa zosowa zanu zonse ndipo akufuna kukuthandizani.

Ikani mavuto anu kwa iye ndipo mudzapeza mtendere. Mukatero, mudzawona momveka bwino zipangizo zomwe muli nazo, zomwe zingakuthandizeni kutuluka mu ngongole. Mukatero, musabwererenso kumeneko, chifukwa Yesu akufuna kuti muyende mu dalitso ndipo ngati munthu wopanda chochita manyazi.

Khalani okhutira ndi zomwe muli nazo tsopano; chifukwa iye anati: Sindidzakusiyani, kapena kukutayani; Aheberi 13:5.




Aroma 13:8

Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:7

Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:6

Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:12

Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:20

Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta; koma wopusa angozimeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:27-28

Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28-30

Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:5

Kusawinda kupambana kuwinda osachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:8

Wochulukitsa chuma chake, pokongoletsa ndi phindu, angokundikira yemwe achitira osauka chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:25-26

Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende. Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumaliza ndiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:26

Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa; ndipo mbumba zake zidalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:26-27

Usakhale wodulirana mpherere, ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake. Ngati ulibe chobwezera kodi achotserenji kama lako pansi pako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:14

Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:15

Woperekera mlendo chikole adzaphwetekwapo; koma wakuda chikole akhala ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:10

Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:1-5

Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole, ngati wapangana kulipirira mlendo, Tulo tapang'ono, kuodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono, ndi kugona; ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota. Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake; zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu. Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa. Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale. wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako, wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako. Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako. Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m'tulo, ndi kulankhula nawe utauka. Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo. Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere. Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali. Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake? Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango. Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse; popeza walowa m'dzanja la mnzako, pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako. Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala; koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake. Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru; wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero. Adzalasidwa nanyozedwa; chitonzo chake sichidzafafanizidwe. Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna, ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango. Sadzalabadira chiombolo chilichonse, sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo. Usaone tulo m'maso mwako, ngakhale kuodzera zikope zako. Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki, ndi mbalame kudzanja la msodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:25

Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:25

Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamuwerengera phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36-37

Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai. Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:27

Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:10-11

Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iliyonse, musamalowa m'nyumba mwake kudzitengera chikole chake. Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituluka nacho chikolecho kwa inu muli pabwalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:12

Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:18

Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina, napereka chikole pamaso pa mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:12

Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:30-31

Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo. Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:7

wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:10-12

Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu. Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:13-14

Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:72

Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golide ndi siliva zikwizikwi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11-13

musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:21

Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11

ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:23-35

Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ake. Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi. Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo. Chifukwa chake kapoloyo anagwada pansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu. Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi chisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole. Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola. Pamenepo kapolo mnzakeyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera. nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole. Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa. Pomwepo mbuye wake anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine; kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni? Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse. Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16

Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:5

Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:7

Wolungama asamalira mlandu wa osauka; koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:1-2

Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale chilekerero. Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu. Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu. Mukagula mbale wanu, Muhebri wamwamuna kapena Muhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi chimodzi; koma chaka chachisanu ndi chiwiri umlole achoke kwanu waufulu. Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu; mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za popondera mphesa, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu. Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino. Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituluka kuchoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu; pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwake, kulikanikiza ndi chitseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzichitanso momwemo ndi adzakazi anu. Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzichita. Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu. Chilekererocho ndichi: okongoletsa onse alekerere chokongoletsa mnansi wake; asachifunse kwa mnansi wake, kapena mbale wake; popeza analalikira chilekerero cha Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:7

ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Zapang'ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:3

Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 10:19

Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10-31

Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu. Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake. Afuna ubweya ndi thonje, nachita mofunitsa ndi manja ake. Akunga zombo za malonda; nakatenga zakudya zake kutali. Aukanso kusanake, napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito. Asinkhasinkha za munda, naugula; naoka mipesa ndi zipatso za manja ake. Amanga m'chuuno mwake ndi mphamvu, nalimbitsa mikono yake. Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku. Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake, nafumbata mtengo wake. Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga? Chiyani mwana wa zowinda zanga? Aolowera chikhato chake osauka; natambasulira aumphawi manja ake. Saopera banja lake chipale chofewa; pakuti banja lake lonse livala mlangali. Adzipangira zimbwi zamawangamawanga; navala bafuta ndi guta wofiirira. Mwamuna wake adziwika kubwalo, pokhala pakati pa akulu a dziko. Asoka malaya abafuta, nawagulitsa; napereka mipango kwa ogulitsa malonda. Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo. Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake. Ayang'anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo. Musapereke mphamvu yako kwa akazi, ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu. Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa. Mumpatse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zimtame kubwalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:23

Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:18

Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa; koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:14-15

Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu. Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:22

Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi; koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:21

Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:1

Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:15

Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:7-9

Zinthu ziwiri ndakupemphani, musandimane izo ndisanamwalire: Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:4

Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:23

Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:45

Ndipo ndidzayenda mwaufulu; popeza ndinafuna malangizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:33

Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:12

Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:27

Wogawira aumphawi sadzasowa; koma wophimba maso ake adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:23

Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:9

Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12

Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:25

Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:24-25

Zilipo zinai zili zazing'ono padziko; koma zipambana kukhala zanzeru: Nyerere ndi mtundu wosalimba, koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:22

Kodi oganizira zoipa sasochera? Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:6-8

Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zao nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; ndipo zituta dzinthu zao m'masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:30-34

Ndinapita pamunda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona, ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-20

Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:2

Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:8

Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:5

Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:19

Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:14

Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36

Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4

Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:17

Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:40

Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:28

Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu; chifundo chichirikiza mpando wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:3

Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:1-2

Monga chipale chofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika, momwemo ulemu suyenera chitsiru. Monga woponya mivi ndi kulasa onse, momwemo wolembera chitsiru, ndi wolembera omwe alikupita panjira. Monga galu abweranso kumasanzi ake, momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake. Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru? Ngakhale chitsiru chidzachenjera koma ameneyo ai. Waulesi ati, Mkango uli panjira, wobangulawo uli m'makwalala. Monga chitseko chikankhikira pa zitsulo za pamphuthu, momwemo waulesi agubuduka pakama pake. Waulesi alonga dzanja lake m'mbale; kumtopetsa kulibweza kukamwa kwake. Waulesi adziyesa wanzeru koposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira. Wakungopita ndi kuvutika ndi ndeu yosakhala yake akunga wogwira makutu a galu. Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa, momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku. Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, moyo wanga ukulambira dzina lanu ndi kukuthokozani chifukwa cha chifundo chanu chosatha. Mwandikomera ine, nthito zonse mwandionetsa kukhulupirika kwanu, chikondi ndi chikhuluriro. Lero ndabwera pamaso panu chifukwa ndikufuna thandizo lanu pa moyo wanga. Mavuto a ngongole andilemetsa, sindingathe kupita patsogolo, ndataya mtendere ndipo ndikusowa pothawira. Ndikukupemphani kuti mundithandize, mundipatse zomwe ndikufunikira kuti ndimalipire ndikhale mfulu ku zinthu izi. Mundikhululukire chifukwa cha zosankha zanga zopanda nzeru ndi kusasamala pazinthu zomwe ndimalonjeza. Mundikhululukire chifukwa cha kupanda kwanga nzeru, sindifuna kukhala chonchi. Sinthani maganizo anga, zochita zanga ndi moyo wanga. Mundipange monga momwe mulili inu mpaka ndikakhale wolungama pamaso panu. Ambuye, ndikukuthokozani chifukwa mwamva pemphero langa, thandizo langa ndi zoperekedwa zidzachokera kumwamba. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa