Yakobo 5:12 - Buku Lopatulika12 Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa. Onani mutuwo |