Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


113 Mau a Mulungu Okhudza Mphamvu ya Kutamanda

113 Mau a Mulungu Okhudza Mphamvu ya Kutamanda

Ndinapangidwa kuti ndimutamande ndi kumulemekeza Mulungu, ndipo pochita zimenezi, ndimapeza madalitso.

M’buku la Machitidwe 16:25-26, timawerenga kuti pakati pa usiku, Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuimba nyimbo zotamanda Mulungu m’ndende, ndipo mwadzidzidzi, chivomezi champhepo chinagwedeza maziko a ndendeyo, zitseko zinatseguka, ndipo maunyolo a akaidi anatuluka. Nkhani imeneyi ikuonetsa mphamvu ya kutamanda Mulungu.

Ngati ine ndikudziwa bwino mphamvu ya kutamanda Mulungu, ndikanayimba kwa Ambuye nthawi zonse. Zilibe kanthu kuti mawu anga ali bwanji; dzina la Yesu liyenera kukwezedwa nthawi zonse.

Pakuvomereza ukulu wake ndi kulengeza mphamvu yake, zitseko zidzatseguka ndipo maunyolo adzasweka m'moyo wanga. Zinthu zidzayenda bwino ngati ndingotamanda Mulungu nthawi zonse.




Masalimo 106:2

Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova, adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:17

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:3

Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:25

Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:47

Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, ndi kutisokolotsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:23

Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:1-2

Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse. ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu. Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake. Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika. Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa. Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu. Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera. Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake. Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu. Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha. Ukani, Yehova, asalimbike munthu; amitundu aweruzidwe pankhope panu. Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:15

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:19

ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 10:21

Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 5:13

Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 5:12

akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:2

Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:1

Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:15

Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:3

Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:11

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 6:20

Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mzinda, yense kumaso kwake; nalanda mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:1

Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 47:1-2

Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa. Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 48:1

Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:23

Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 57:7-9

Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza. Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze! Ndidzauka ndekha mamawa. Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:3-4

Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:1-2

Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva. Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa. Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, zimene inazitchula milomo yanga, ndinazinena pakamwa panga posautsika ine. Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi. Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga. Ndinamfuulira Iye pakamwa panga, ndipo ndinamkuza ndi lilime langa. Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera. Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa. Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:8

M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:1-2

Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri, kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:1-2

Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika. Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera. Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi. Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:4

Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:1-2

Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:1-2

Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye. ndipo anachiimikira Yakobo, chikhale malemba, chikhale chipangano chosatha kwa Israele. Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholowa chako; pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo; nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena. Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa. Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga. Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate. Anawatsogozeratu munthu; anamgulitsa Yosefe akhale kapolo: Anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka mu unyolo; kufikira nyengo yakuchitika maneno ake; mau a Yehova anamuyesa. Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:1

Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:3

Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:1

Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 117:1-2

Lemekezani Yehova, amitundu onse; muimbireni, anthu onse. Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu; ndi choonadi cha Yehova nchosatha. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:24

Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:164

Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:1-2

Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu. Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:1-3

Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse. Yehova agwiriziza onse akugwa, naongoletsa onse owerama. Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao. Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse. Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa. Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga. Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi. Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:1-2

Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga. Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:1

Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:1-6

Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:2

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:50

Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:23-25

Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu, zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:34

Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:10-13

Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya. Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 5:13-14

Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova; ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:21-22

Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha. Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 3:11

Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 9:5-6

Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse. Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 1:21

nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:4-5

Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:1

Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:10

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:7

Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 20:13

Muimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Habakuku 3:17-18

Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao; koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 9:9

Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:9

Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:16

nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:30

Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 14:26

Ndipo ataimba nyimbo, anatuluka, namuka kuphiri la Azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:46-47

Ndipo Maria anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye, ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:13-14

Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena, Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:37-38

Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona; nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:23-24

Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:46-47

Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:25-26

Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva; ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:9

ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:26

Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:6

kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:12

kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:18-20

Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:11

odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:4

Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:12

ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16-17

Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:16-18

Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:17

Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:12

Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:19-22

Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu, Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:28

Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3

Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:11

akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:11

Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:18

Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:1

Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:24-25

Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera, kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:6

natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 5:12-13

akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko. Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:17

nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:10-11

Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku. Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 15:3-4

Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:1

Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:5-6

Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu. Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:1-2

Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga. Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 98:4-6

Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze; ndi zeze ndi mau a salimo. Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova, ndi mbetete ndi liu la lipenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:9

Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:10

Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:3

Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova pa nyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 2:20

Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:13

anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:1-3

Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao. Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:6

Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao, ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvu Zonse! Ndikubwerera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, Inu nokha ndinu Woyenera kutambasula ulemu ndi kupembedzedwa konse. Atate Woyera, chifuniro chanu ndichakuti mitima yathu ikhale yodzala ndi chiyamiko mosasamala kanthu za mavuto kapena zomwe tikukumana nazo, ndipo kuti kuyamika kwathu kukhale kwamphamvu kwambiri, pakuti pomwepo mphamvu zanu zodabwitsa zimaonekera ndipo zinthu zodabwitsa zimachitika. Ndithudi, komwe kuli Mzimu wa Ambuye kuli kumasuka, machiritso ndi zodabwitsa m'miyoyo yathu, monga momwe zinachitikira ndi Paulo ndi Sila omwe pakati pa nyimbo zawo panachitika chivomezi chomwe chinagwedeza maziko a ndende ndipo nthawi yomweyo zitseko zinatseguka ndipo maunyolo awo anamasulidwa. Atate Woyera, ndikufuna kukhala wogwira ntchito mumphamvu zanu osati wowonera chabe, ndithandizeni kuzindikira kuti pali anthu ozungulira ine omwe ali m'ndende, okhumudwa, ndipo chifuniro chanu ndichakuti nawonso akhudzidwe ndi mphamvu zomwezo, chifukuti kuyamika kwanga kwa Inu kumadutsa malire ndipo ndi chida champhamvu chosweka maunyolo onse a mdani. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa