Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 7:3 - Buku Lopatulika

3 Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova pa nyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova panyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndipo Aisraele onse ataona moto wotsika kumwambawo, pamodzi ndi ulemerero wa Chauta m'Nyumba ya Chauta ija, adaŵerama, nazyolikitsa nkhope zao pansi, ndipo adapembedza nathokoza Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Aisraeli onse ataona moto ukuchokera kumwamba ndi ulemerero wa Yehova pamwamba pa Nyumba ya Mulungu, anagwada poyalidwa miyalapo ndipo anagunditsa nkhope zawo pansi, ndi kulambira ndi kutamanda Yehova, ponena kuti, “Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala chikhalire”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 7:3
26 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.


Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.


ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;


Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala mu Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.


Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.


Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza.


Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.


Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.


Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;


Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.


Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti chifundo chake nchosatha.


Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.


Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.


Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.


Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.


Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.


mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.


Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.


Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israele.


Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?


Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa