2 Mbiri 7:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Tsono ansembe sadathe kuloŵa m'Nyumbamo, popeza kuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'menemo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Ansembe sanathe kulowa mʼNyumba ya Mulungu chifukwa munadzaza ulemerero wa Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;