Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


107 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Yesu

107 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Yesu

Ndili ndi uthenga wabwino kwambiri kwa inu lero. Mu Colose 2:13-15, tikuwona mphamvu ya Khristu pa zoipa zonse, machimo onse, ndi maufumu onse. Baibulo limati, "Inu amene munali akufa m’machimo anu ndi m’kusadulidwa kwa thupi lanu, Iye anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, anakhululukira machimo anu onse; anathetsa chikalata cha milandu chimene chinali chotitsutsana, nachichotsa pakati, nachikhomera pa mtanda; ndipo atavula maufumu ndi maulamuliro, anawaonetsa poyera, napambana pa iwo mwa mtanda."

Taganizirani zimenezi! Khristu anakhululukira machimo anu onse! Anagonjetsa mphamvu za mdima! Chifukwa cha nsembe yake pa mtanda, muli ndi ufulu ndi moyo. Tiyenera kukumbukira nthawi zonse mphamvu imeneyi ndi ulamuliro umene uli wa Khristu.

Mphamvu ndi ulamuliro umenewu umalemekeza Yesu Khristu, amene analemekeza Atate. Ndipo Atate amatiuza kuti tionetse mphamvu imeneyi pano padziko lapansi, m’mipingo yathu, ndi m’mitundu yonse. Tiyeni tipite ndi kulalikira uthenga wabwino wa chipulumutso kwa munthu aliyense. Mulungu akhale nanu.




Luka 6:19

ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:6

Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:27

Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:23-24

Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu. Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:18

Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:3

ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:28-29

Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:29

pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:17

Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:3

Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:1

Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:16-17

Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse; kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:25

kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:26-27

Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu. Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:4

amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:31

Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:17

Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:24

koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:35

Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:27

Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 14:25-27

Ndipo pa ulonda wachinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja. Koma m'mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo anafuula ndi mantha. Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 14:35-36

Ndipo m'mene amuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse kudziko lonse lozungulira, nadza nao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda; ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:30-31

Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:18-19

Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo. Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:20-21

Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:18-20

Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula padziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba. Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18

Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:27-28

Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye. Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:10-11

pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze. Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:39-41

Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu. ndipo kunali, m'kufesa kwake, zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndi mbalame zinadza ndi kuzitha kudya. Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi? Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:1-20

Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa. Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko. Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri. Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho. Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo. Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m'malire ao. Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo. Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:25-34

Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula, m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake. Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa. Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake adaphwa; ndipo anazindikira m'thupi kuti anachiritsidwa chivutiko chake. amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo; Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga? Ndipo ophunzira ake ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lilikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani? Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi. Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse. Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:41-42

Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:7

Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:56

Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 8:6-9

Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo. Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso. Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri. Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:23

Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:27

Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17-18

Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano; adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18-19

Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika, kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:36-37

Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka. Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:12-13

Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza. Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:24

Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:17-19

Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao; ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa, ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:14-15

Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:21

Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:25

Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m'kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:43-48

Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chovala chake; ndipo pomwepo nthenda yake inaleka. Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana. Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine. Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo. Ndipo Iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:1-2

Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda. Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida. Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa. Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno. Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya. Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu. Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo. Ndipo Iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo. Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri. Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale. Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:11

Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:43

Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:17-19

Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:27

Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:49

Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:14

Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 2:7-9

Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, ndendende. Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwa mkulu wa phwando. Ndipo anapita nao. Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwe kumene anachokera (koma atumiki amene adatunga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:35

Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:21

Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24-25

Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:35

Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:63

Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:12

Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:36

Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:10

Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:28-30

Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa. Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate. Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja. Ine ndi Atate ndife amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:6

Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:12-14

Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate. Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:5

Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:2

monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:22

Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:36

Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6

Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:10

zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:30

m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:12

Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:18

Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:17

Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:11

Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:34

ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso padzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:14

koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:19-21

ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba, Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. imene anachititsa mwa Khristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa padzanja lake lamanja m'zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-17

kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:16-17

pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:19-20

Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire, kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a mu Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu. mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:5

kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:9

amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:15-17

Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa; komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha. Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:10

koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:14-15

Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:15-16

Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:24

amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:18

Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:8

iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4-5

Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:8

Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Wabwino, Wachifundo ndipo mwakhululukira moyo wanga. Atate Woyera, ndikubwerera kwa Inu, chifukwa Inu nokha muli ndi Mphamvu yopulumutsa, kuchiritsa ndi kumasula. Ndikupemphani kuti mundidzaze ndi kukhalapo kwanu kwaulemerero ndipo Mphamvu yanu iwonekere pa moyo wanga ndi wa banja langa kuti tonse pamodzi tifunitsitse kukwaniritsa cholinga chimene munakonzeratu ife. Ndithandizeni kutsanzira chikhulupiriro chanu kulikonse kumene ndikupita ndipo kukhalapo ndi Mphamvu ya Mzimu Woyera wanu kuwonekere m'miyoyo ya achinyamata, achikulire, okalamba ndi onse amene ali pafupi ndi ine. Ndidziwitseni kuyenda monga momwe Inu munayendera, muchiritsa odwala, kumasula ogwidwa ndi kuchiritsa onse oponderezedwa. Ndithandizeni kukhala paubwenzi wolimba ndi Inu kuti ndiphunzire kugonjetsa mantha ndi kudzutsa mphamvu (dunamis) imene munaiika mwa ine. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa