Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:24 - Buku Lopatulika

24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:24
26 Mawu Ofanana  

Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.


Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.


Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa Munthu ndiye yani?


Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:


Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.


Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.


Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye.


Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?


Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.


Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka.


Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau aakulu, Lazaro, tuluka.


monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.


Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala mu Mwambayo.


ndipo anampatsa Iye mphamvu ya kuchita mlandu, pakuti ali Mwana wa Munthu.


anati ndi mau aakulu, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.


Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.


Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.


Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.


ndipo pakati pa zoikaponyalizo wina wonga Mwana wa Munthu atavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa