Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Pomwepo wodwalayo adadzukadi onse akupenya, ndipo adatenga machira aja amene adaagonapo, namapita kwao akutamanda Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:25
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.


Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.


Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinazione ndi kale lonse.


Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.


Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.


Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.


Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa