Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:36 - Buku Lopatulika

36 Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 “Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 “Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:36
25 Mawu Ofanana  

Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele;


Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda;


Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israele ndi za nyumba ya Yuda.


Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima.


Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.


Chifukwa chake nena kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israele, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.


Dziwani kuti sindichita ichi chifukwa cha inu, ati Ambuye Yehova; chitani manyazi, dodomani, chifukwa cha njira zanu, nyumba ya Israele inu.


Ndipo dziko lake la mzindawo mulipereke la mikono zikwi zisanu kupingasa kwake, ndi mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, pa mbali ya chipereko chopatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israele.


Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.


pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.


kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.


nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.


Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa