Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 3:35 - Buku Lopatulika

35 Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Mulungu Atate amakonda Mwana wake, ndipo adaika zonse m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 3:35
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m'dziko lonse la Ejipito.


Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.


Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.


Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri; ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse;


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.


Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'chikondi changa.


monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.


Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.


ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.


Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe.


Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana;


Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.


ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo


koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa