Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 2:22 - Buku Lopatulika

22 Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 “Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 2:22
42 Mawu Ofanana  

Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.


Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.


nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.


Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.


Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo mu Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?


Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.


Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine.


Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.


Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m'mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni.


Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.


Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.


Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.


Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.


Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?


Ngati uyu sanachokere kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.


Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.


Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.


Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;


Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi.


nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao mu Kachisi, nadetsa malo ano oyera.


Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitike m'tseri.


Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.


Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?


Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.


zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.


pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa