Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:10 - Buku Lopatulika

10 zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mudziŵetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyu akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:10
16 Mawu Ofanana  

Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.


nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.


amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa