Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:11 - Buku Lopatulika

11 Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Za Yesuyo mau a Mulungu akuti, “ ‘Mwala umene inu amisiri omanga nyumba mudaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Iye ndi “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana, umenewo wasanduka mwala wa pa ngodya!’

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:11
20 Mawu Ofanana  

Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.


Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.


Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,


Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa