Marko 6:56 - Buku Lopatulika56 Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201456 Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'milaga, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa56 Kulikonse kumene Yesu ankapita, ku midzi ndi ku mizinda, anthu ankadzakhazika odwala pa mabwalo. Ankamupempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero56 Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira. Onani mutuwo |