Chikondi cha Mulungu chimapita patsogolo pa chilichonse, ndi chikondi choyera komanso chodzala ndi chifundo, chokonzeka kupereka zonse chifukwa cha iwe. Sichimayang'ana pa zomwe ukuchita, koma chimachokera mu mtima woyera wa Mulungu amene anatumiza Mwana wake yekhayo kuti adzafere chifukwa cha iwe, kuti ukhale pa ubale naye monga atate alili ndi mwana wake.
Kale, tonse tinali kutali ndi Mulungu chifukwa cha machimo athu ndi zofooka zathu, koma polandira Yesu m'mitima mwathu, takhala ana a Mulungu. Yamikira zonse zomwe Mulungu wachita kuti mukhale pafupi naye, yamikira chikondi chake chopanda kufanana ndipo khalani moyo woyera pamaso pake.
Khalani mwana amene angamunyasitse Mulungu, amene angamupangitse kumwetulira kuchokera kumwamba akamakuona. Mukonde Mulungu ndi mtima wako wonse, ukhale ndi chikhulupiriro chomuuza mavuto ako onse, kuti umupemphe zomwe ukufuna, kuti umusonyeze zofooka zako, chifukwa iye sadzakuseka; m'malomwake, amakukonda kwambiri moti amangofuna kuti umudziwe ndi kumumvera nthawi zonse.
Mulungu ndi Atate wabwino kwambiri, wachifundo, woleza mtima, amene amalanga ndi kukonza, komanso amadziwa kuyamikira zabwino zomwe umachita. Ndipo kumbukira, ngakhale makolo ako atakukana, Yehova sadzakukana, suli wekha, ali nawe kuti akuteteze, akusamalire ndi kukuuzani kuti: "Usachite mantha, ndikuthandiza." Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse, amene ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito mwa onse, ndipo ali mwa onse. Aefeso 4:6.
Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.
Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.
Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.
Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.
Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse,
Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.
Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.
Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate! Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.
amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu;
Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.
Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.
Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.
Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga.
Mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuona Iye.
Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!
Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israele satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wachikhalire ndi dzina lanu.
Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau aakulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.
Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.
Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja; Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake. kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa. Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate. Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja. Ine ndi Atate ndife amodzi.
ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye; pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.
Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?
Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,
Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu. ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.
Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.
Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.
Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani?
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate, amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alitcha dzina,