Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 20:17 - Buku Lopatulika

17 Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Yesu adamuuza kuti, “Usandigwire, pakuti sindinakwerebe kupita kwa Atate. Koma pita kwa abale anga, ukaŵauze kuti, ‘Ndikukwera kupita kwa Atate anga, omwe ali Atate anunso, Mulungu wanga, yemwe ali Mulungu wanunso.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 20:17
48 Mawu Ofanana  

Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.


Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.


Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.


Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.


Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;


Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.


Kachisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.


Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.


Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.


Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.


simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.


Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.


Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.


Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine;


Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.


Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.


Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.


Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;


ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.


Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la mu Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mzinda.


Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa