Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Masalimo 9:2 - Buku Lopatulika Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu; Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba. |
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.
Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.
Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.
Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.
Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;