Masalimo 83:18 - Buku Lopatulika18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Adziŵe kuti Inu nokha, amene dzina lanu ndinu Chauta, ndinu Wopambanazonse wolamulira dziko lonse lapansi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi. Onani mutuwo |
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.