Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 83 - Buku Lopatulika


Amitundu apangana kuononga Aisraele. Apempha Mulungu awalanditse
Nyimbo. Salimo la Asafu.

1 Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.

2 Pakuti taonani, adani anu apokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.

3 Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu.

4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.

5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu.

6 Mahema a Edomu ndi a Aismaele; Mowabu ndi Ahagiri;

7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.

8 Asiriya anaphatikana nao; anakhala dzanja la ana a Loti.

9 Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,

10 amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda.

11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu; mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,

12 amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.

13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu; ngati ziputu zomka ndi mphepo.

14 Monga moto upsereza nkhalango, ndi monga lawi liyatsa mapiri.

15 Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.

16 Achititseni manyazi pankhope pao; kuti afune dzina lanu, Yehova.

17 Achite manyazi, naopsedwe kosatha; ndipo asokonezeke, naonongeke.

18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa