Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 83:14 - Buku Lopatulika

14 Monga moto upsereza nkhalango, ndi monga lawi liyatsa mapiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Monga moto upsereza nkhalango, ndi monga lawi liyatsa mapiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Monga momwe moto umatenthera nkhalango, monga momwe malaŵi amayakira pa mapiri,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 83:14
11 Mawu Ofanana  

Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo, ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?


Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.


Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.


Pakuti kuchimwa kwayaka ngati moto kumaliza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m'nkhalango ya m'thengo, ndipo zifuka chapamwamba, m'mitambo yautsi yochindikira.


Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.


Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa