Masalimo 16:1 - Buku Lopatulika Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndisungeni Inu Mulungu, pakuti ine ndimathawira kwa Inu. |
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye.
Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu; mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;
ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.
Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.
koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;
Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.